Quantcast

Malawi Opens the Warm Heart of Africa to whl.travel

 • whl.travel
 • 22 July 2010

SEE BELOW FOR THIS MESSAGE IN CHICHEWA / ONANI UTHENGAWU PANSIPA MU CHICHEWA

Malawi is one of Africa’s little known treasures. Surrounded by the much larger countries of Mozambique, Tanzania and Zambia, Malawi is a narrow nation, only slightly smaller than North Korea, that runs north to south along the Great Rift Valley. It’s been called ‘the warm heart of Africa,’ something you will know is true once you hear your first mwalandiridwa (welcome).

Hippos laze in the Shire River of Malawi’s Liwonde National Park

Hippos laze in the Shire River, which runs along the western border of Malawi’s most prolific wildlife park, Liwonde National Park

The diversity of landscapes in Malawi is truly astonishing for such a small country. Elevations range from just above sea level to 3,000 metres at Mount Mulanje, which can be explored on a hike or, for the more daring, on a summit trip. Nine game reserves and national parks await nature and wildlife aficionados and are best experienced on a Malawi tour or safari, easily accomplished from the capital city of Lilongwe or the commercial centre of Blantyre. Also within easy reach are Malawi’s two UNESCO-recognised World Heritage Sites: Lake Malawi National Park, known for its endemic fish populations, and the culturally important Chongoni Rock Art Area, which dates back to the late Iron Age.

Amidst all the other sights, Malawi’s most famous natural attraction is the spectacular freshwater Lake Malawi, stretching for 584 km along nearly half of the length of the country. Its delightful waters are the focus of many activities, like PADI diving courses, snorkelling and kayaking, although landlubbers too may enjoy it from the shore on a horse’s back (followed by a swim with the horses) or in the saddle of a bicycle.

As perfect bases from which to discover Malawi’s myriad attractions, a careful selection of hotels, safari lodges and campsites round out the offerings provided by www.explore-malawi.com, whl.travel’s first destination portal in Malawi.

This Web portal now links travellers to local specialists, The Responsible Safari Company, on whose behalf Kate Ward says, “We’re thrilled to be part of such an exciting new initiative that offers independent travellers access to a quicker, easier and cheaper way to book their travel in Malawi. The combination of online bookings with local-travel initiatives provides travellers with a unique opportunity to tailor-make their own experiences. With its diversity of plateaus, mountains and national parks, in combination with the stunning shores of Lake Malawi, Malawi is an extraordinary destination and we hope that this new site will play a part in the development of the country’s tourism industry.”

———-

IN CHICHEWA / MU CHICHEWA:

Malawi ndidziko limodzi laling’ono lodziwika mu Afirika ndipo lidazunguliridwa ndi mayiko ena akulu monga Mozambique, Tanzania ndi Zambia. Dziko la Malawi ndilocheperako kuyerekeza ndi dziko la North Korea ndipo likupezeka kuchokera ku mpoto kukafika ku mwera kwa chigwa chachikulu. Dziko la Malawi limadziwika ngati ‘Dziko la anthu amsangala mu Afirika,’ mungavomereze izi pokumva mawu oyamba akuti mwalandiridwa.

The Gule Wamkulu, or Great Dance, is a masked ritual and symbolic dance performed in Malaw

The Gule Wamkulu, or Great Dance, is a masked ritual and symbolic dance performed in Malawi at important ceremonies and funerals

Chilengedwe cha dziko la Malawi ndichozwizwitsa poyerekezera ndi kuchepa kwa dzikoli ndipo mitunda yake ndiyokwera kufikira mamitara 3,000 pa phiri la Mulanje lomwe ndilotheka kukwera ndi miyendo ndikufika pamwamba penipeni pa phiriri. Ku Malawi kuli malo asanu ndi anayi wosungiramo nyama zakuntchire omwe ndi wokongola mododometsa ndipo ndikotheka kukawona malowa kupyolera m’maulaendo osiyanasiyana ponyamukira m’chigawo chapakati ku Lilongwe kapena chigawo chakumwera ku Blantyre. Malo ena osavuta kufikako ndi malo awiri a UNISCO ku Malawi omwe ndi: Lake Malawi National Park, malowa amadziwika ndi mitundu yosiyanasiyana ya nsomba yochuluka kuposa kulikonse pa dziko lapansi. Malo ena ofunikira kwambiri makamaka kuchikhalidwe chathu ndi a Chingoni Rock Art Area omwe adalipo angakhale nthawi yomwe anthu adayamba kuphunzira kugwiritsa ntchito zitsulo (Iron Age).

Nyanja Ya Malawi yomwe ili ndi madzi oyera bwino ndiyodziwika kwambiri kuposa malo ena onse azachilengedwe ku Malawi ndipo nyanjayi ndiyayitali kufikira makilomita 584 – kutalika pafupifupi theka la dziko lonse. Zochitika zosiyanasiyana ndi zambiri munyanjayi, monga: maphunziro azosambira kukawona nsomba, zomera ndi zonse zopezeka pansi pa nyanja, zosambira kukawona nsomba, zomera ndi zonse zopezeka pansi pa Nyanja ndiponso kuyendetsa bwato za pulasitiki, ngakhale anthu amene sadziwa ndipo sakonda masewero a m’madzi ali ndi mwayi osangalala kunyanjaku pokwera a bulu mbali mwa nyanja (kenako kulowa m’madzi ali pa mnsana pa bulu) kapena kukwera njinga.

Malo ogulitsirapo zokopa alendowa ndiwoyamba ku Malawi kukhazikitsidwa ndi a whl.travel ndipo ndiwothandiza kuti mudziwe zinthu zopatsa chikoka za ku Malawi, malo monga mahotela ndi maloji aliponso ndipo adasankhidwa mwachifatse www.explore-malawi.com.

Malo awa ogulitsirapo malonda azokopa alendo tsopano amalumikiza ogula am’mayiko osiyasiyana ndi ogulitsa aku Malawi, The Responsible Safari Company, ndipo woyimira kampaniyi a Kate Ward akuti “Ndife osangalala koposa potenga nawo mbali munjira yatsopanoyi yogulitsira malonda okopa alendo yomwe idzilola alendo kugwiritsa ntchito njira yachangu, yosavuta ndiponso yotsika mtengo pomwe akonzekera ulendo wawo wodzawona Malawi. Kagulidwe aka kamalaonda okopa alendo kuphatikiza ndi mchitidwe wa zokopa alendo mogwirizana ndi chikhalidwe cha m’dela zimapatsa alendo mwayi opambana kuti awone ndikutenga nawo mbali m’zachikhalidwe chosiyana ndi chawo. Malawi ndi dziko lododometsa chifukwa cha zachilengedwe zosiyanasiyana monga mitunda, magomo ndi malo osungiramo nyama zakutchire omwe amapezeka m’dzikoli ndipo tikukhulupirira kuti njira yatsopanoyi yithandiza kutukula ntchito zokopa alendo ku Malawi.”

Related Posts Plugin for WordPress, Blogger...
Spread The Word:
 • Print
 • Digg
 • StumbleUpon
 • del.icio.us
 • Facebook
 • Yahoo! Buzz
 • Twitter
 • Google Bookmarks
 • email
 • LinkedIn
 • Posterous
 • Reddit

adventure travel, Africa, Eastern Africa, ecotours, forests & jungles, lakes, Malawi, national parks, new local connections, responsible travel, WHL Group news, whl.travel,

Leave a Reply